Mavesi a m'Baibulo Onena za Nsanje
Mavesi 7 a m'Baibulo onena za Nsanje oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Pakuti pamene pali kaduka ndi kudzikonda pomweponso pamakhala chisokonezo ndi zochitika zoyipa zonse.
Mtima wodekha umapatsa thupi moyo, koma nsanje imawoletsa mafupa.
Tisakhale odzitukumula, oputana ndi ochitirana nsanje.
Chikondi nʼcholeza mtima, chikondi nʼchokoma mtima, chilibe nsanje, sichidzikuza, sichidzitamandira.
Choncho, lekani zoyipa zonse, chinyengo chilichonse, chiphamaso, nsanje ndi kusinjirira kulikonse.
Nthawi ina tinali opusa, osamvera, onamizidwa ndi omangidwa ndi zilakolako ndi zokondweretsa zamitundumitundu. Tinkakhala moyo wadumbo ndi wakaduka, odedwa ndiponso odana wina ndi mnzake.
Pakuti ndinkachitira nsanje odzitamandira, pamene ndinaona mtendere wa anthu oyipa.