Mavesi a m'Baibulo Onena za Kuzondana

Mavesi 6 a m'Baibulo onena za Kuzondana oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Ahebri 12:15

Yangʼanitsitsani kuti wina aliyense asachiphonye chisomo cha Mulungu ndiponso kuti pasaphuke muzu wamkwiyo umene udzabweretsa mavuto ndi kudetsa ambiri.

02 Aefeso 4:31

Chotsani kuzondana, ukali ndi kupsa mtima, chiwawa ndi kuyankhula zachipongwe, pamodzi ndi choyipa chilichonse.

03 Aefeso 4:32

Mukomerane mtima ndi kuchitirana chifundo wina ndi mnzake. Khululukiranani wina ndi mnzake, monga momwe Mulungu anakukhululukirani mwa Khristu.

04 Akolose 3:13

Mulezerane mtima ndipo muzikhululukirana ngati wina ali ndi chifukwa ndi mnzake. Muzikhululukirana monga Ambuye anakhululukira inu.

05 Ahebri 12:14-15

Yesetsani kukhala pa mtendere ndi anthu onse ndi kukhala oyera mtima, pakuti popanda chiyero palibe ndi mmodzi yemwe adzaona Ambuye. Yangʼanitsitsani kuti wina aliyense asachiphonye chisomo cha Mulungu ndiponso kuti pasaphuke muzu wamkwiyo umene udzabweretsa mavuto ndi kudetsa ambiri.

06 1 Akorinto 13:5

Chikondi chilibe mwano, sichodzikonda, sichipsa mtima msanga, sichisunga mangawa.

Mitu yofanana