Mavesi a m'Baibulo Onena za Tchimo
Mavesi 10 a m'Baibulo onena za Tchimo oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
pakuti onse anachimwa naperewera pa ulemerero wa Mulungu
Pakuti malipiro a tchimo ndi imfa, koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Koma tikavomereza machimo athu, Iye ndi wokhulupirika ndi wolungama ndipo adzatikhululukira machimo athu, nadzatiyeretsa ndi kutichotsera chosalungama chilichonse.
Ife tonse, ngati nkhosa, tasochera, aliyense mwa ife akungodziyendera; ndipo Yehova wamusenzetsa zoyipa zathu zonse.
Aliyense amene amadziwa zabwino zimene amayenera kuchita koma osazichita, ndiye kuti wachimwa.
Tikanena kuti tilibe tchimo, tikudzinyenga tokha ndipo mwa ife mulibe choonadi.
Choncho monga momwe tchimo linalowa mʼdziko lapansi kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mu tchimo, mʼnjirayi imfa inafika kwa anthu onse pakuti onse anachimwa.
Zoonadi ine ndinali wochimwa pomwe ndimabadwa, wochimwa kuyambira pa nthawi imene amayi anga anakhala woyembekezera ine.
Musanamizidwe: nʼkosatheka kupusitsa Mulungu. Munthu amakolola zimene wafesa. Pakuti amene amafesa zokondweretsa thupi lake la uchimo, kuchokera ku khalidwe limenelo adzakolola chiwonongeko; amene amafesa zokondweretsa Mzimu, kuchokera kwa Mzimu adzakolola moyo wosatha.
Tchimo silidzakhalanso ndi mphamvu pa inu, chifukwa Malamulo sakulamulira moyo wanu koma chisomo.