Mavesi a m'Baibulo Onena za Kunyada

Mavesi 13 a m'Baibulo onena za Kunyada oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Miyambo 16:18

Kunyada kumafikitsa ku chiwonongeko, ndipo munthu wodzikuza adzagwa.

02 Miyambo 11:2

Kunyada kukalowa, pamafikanso manyazi, koma pamene pali kudzichepetsa pameneponso pali nzeru.

03 Yakobo 4:6

Koma amatipatsa chisomo chochuluka. Nʼchifukwa chake Malemba amati, “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma apereka chisomo kwa odzichepetsa.”

04 Miyambo 16:5

Munthu aliyense wodzikuza amamunyansa Yehova. Koma dziwani izi: Iwo sadzakhala osalangidwa.

05 1 Petro 5:5

Momwemonso, inu anyamata gonjerani amene ndi akulu. Inu nonse mukhale odzichepetsa kuti mutumikirane, chifukwa, “Mulungu amatsutsana nawo odzikuza, koma amapereka chisomo kwa odzichepetsa.”

06 Miyambo 8:13

Kuopa Yehova ndiko kudana ndi zoyipa. Ine ndimadana ndi kunyada, kudzitama, kuchita zoyipa, ndiponso kuyankhula zonyenga.

07 Miyambo 18:12

Chiwonongeko chisanafike, mtima wa munthu umakhala wonyada, koma ulemu umatsatira kudzichepetsa.

08 Miyambo 29:23

Kunyada kwa munthu kudzamutsitsa, koma munthu wodzichepetsa amalandira ulemu.

09 Yesaya 2:11

Kudzikuza kwa anthu kudzatha, ndipo kudzitama kwa anthu kudzawonongedwa; Yehova yekha ndiye adzapatsidwe ulemu pa tsiku limenelo.

10 Luka 14:11

Pakuti aliyense wodzikuza adzamuchepetsa, ndipo aliyense wodzichepetsa adzamukweza.”

11 Agalatiya 6:3

Ngati wina adziyesa kanthu pamene iyeyo sali kanthu konse, akudzinamiza yekha.

12 Aroma 12:3

Chifukwa cha chisomo chopatsidwa kwa ine, ndinena kwa aliyense wa inu kuti musadziyenereze nokha kuposa mmene mulili. Koma mudziganizire nokha modzichepetsa, molingana ndi muyeso wa chikhulupiriro chimene Mulungu wakupatsani.

13 Miyambo 3:34

Anthu onyoza, Iye amawanyoza, koma amakomera mtima anthu odzichepetsa.

Mitu yofanana