Mavesi a m'Baibulo Onena za Ndisanthuleni, Mulungu
Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Ndisanthuleni, Mulungu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Santhuleni, Inu Mulungu ndipo mudziwe mtima wanga; Yeseni ndipo mudziwe zolingalira zanga.
Onani ngati muli mayendedwe aliwonse oyipa mwa ine, ndipo munditsogolere mʼnjira yanu yamuyaya.
Ndani angathe kudziwa zolakwa zake? Mundikhululukire zolakwa zanga zobisika.
Mulenge mʼkati mwanga mtima woyera Inu Mulungu ndi kukonzanso mzimu wokhazikika mwa ine.
Patseni mayeso, Inu Yehova ndipo ndiyeseni, santhulani mtima wanga ndi maganizo anga;
Inu Mulungu wolungama, amene mumasanthula maganizo ndi mitima, thetsani chiwawa cha anthu oyipa ndipo wolungama akhale motetezedwa.
Ngakhale Inu mutafufuza mtima wanga ndi kundisanthula usiku, ngakhale mutandiyesa, simudzapeza kanthu; Ine ndatsimikiza kuti pakamwa panga sipadzachimwa.
“Ine Yehova ndimafufuza mtima ndi kuyesa maganizo, ndimachitira munthu aliyense molingana ndi makhalidwe ake ndiponso moyenera ntchito zake.”
“Ndipo iwe mwana wanga Solomoni, umvere Mulungu wa abambo ako, umutumikire ndi mtima wodzipereka kwathunthu ndi mtima wako wonse, pakuti Yehova amasanthula mtima wa aliyense, ndipo amadziwa maganizo aliwonse a munthu. Ngati ufunafuna Yehova, Iye adzapezeka; koma ngati umutaya, Iye adzakukana kwamuyaya.
kodi Mulungu wathu sakanazidziwa zimenezi, pakuti Iye amadziwa zinsinsi zamumtima?
Paja Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amalowa mpaka molumikizirana moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana fundo ndi mafuta a mʼmafupa. Amaweruza malingaliro ndi zokhumba za mʼmitima.