Mavesi a m'Baibulo Onena za Tetezani Mtima Wanu

Mavesi 10 a m'Baibulo onena za Tetezani Mtima Wanu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Miyambo 4:23

Ndipotu mtima wako uziwuyangʼanira bwino ndithu pakuti ndiwo magwero a moyo.

02 Afilipi 4:7

Ndipo mtendere wa Mulungu, umene upambana nzeru zonse udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

03 Mateyu 12:34

Ana anjoka inu, woyipa inu, mungathe bwanji kuyankhula kanthu kalikonse kabwino? Pakuti pakamwa pamayankhula zosefuka kuchokera mu mtima.

04 Miyambo 4:24-25

Usiyiretu kuyankhula zokhotakhota; ndipo ulekeretu kuyankhula zinthu zonyansa. Maso ako ayangʼane patsogolo; uziyangʼana kutsogolo molunjika.

05 Masalimo 119:11

Ndasunga mawu anu mu mtima mwanga kuti ndisakuchimwireni.

06 Miyambo 23:7

paja iye ndi munthu amene nthawi zonse amaganizira za mtengo wake ngakhale amati kwa iwe, “Idya ndi kumwa,” koma sakondweretsedwa nawe.

07 Luka 6:45

Munthu wabwino amatulutsa zinthu zabwino zosungidwa mu mtima mwake, koma munthu oyipa amatulutsa zinthu zoyipa zosungidwa mu mtima mwake. Pakamwa pake pamayankhula zimene zadzaza mu mtima mwake.

08 Masalimo 51:10

Mulenge mʼkati mwanga mtima woyera Inu Mulungu ndi kukonzanso mzimu wokhazikika mwa ine.

09 Deuteronomo 6:6

Malamulo amene ndakupatsani lero ayenera kukhala mu mtima mwanu.

10 Miyambo 4:21

Usayiwale malangizo angawa, koma uwasunge mu mtima mwako.

Mitu yofanana