Mavesi a m'Baibulo Onena za Kukana Mdyerekezi
Mavesi 10 a m'Baibulo onena za Kukana Mdyerekezi oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Dziperekeni nokha kwa Mulungu. Mukaneni Mdierekezi ndipo adzakuthawani.
Khalani odziretsa ndi atcheru. Mdani wanu mdierekezi amayendayenda monga mkango wobangula kufunafuna wina kuti amumeze. Mukaneni iye, ndipo mukhazikike mʼchikhulupiriro, chifukwa mukudziwa kuti abale anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso akumva zowawa zomwezi.
Valani zida zonse za Mulungu kuti muthe kuyima ndi kukana machenjerero a Satana.
kupewa kuti Satana angapezere mpata pa ife, pajatu timadziwa machenjerero ake.
Yesu anati kwa iye, “Choka Satana! Zalembedwa, ‘Pembedza Yehova Mulungu wako ndi kumutumikira Iye yekha.’ ”
Choncho valani zida zonse za Mulungu, kuti pamene tsiku loyipa kwambiri lifika, mudzathe kuyima chilili, ndipo mutatha kuchita zonse, mudzayimabe mwamphamvu.
Mukaneni iye, ndipo mukhazikike mʼchikhulupiriro, chifukwa mukudziwa kuti abale anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso akumva zowawa zomwezi.
Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa: ‘Pembedza Yehova Mulungu wako ndi kumutumikira Iye yekha.’ ”
Musamupatse mpata Satana.
Inu ana okondedwa, ndinu ochokera kwa Mulungu ndipo mwawagonjetsa aneneri onyengawa, chifukwa Iye amene ali mwa inu ndi wamkulu kuposa amene ali mʼdziko lapansi.