Mavesi a m'Baibulo Onena za Olandiridwa mwa Wokondedwayo

Mavesi 13 a m'Baibulo onena za Olandiridwa mwa Wokondedwayo oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Aefeso 1:6

Anachita zimenezi kuti tiziyamika ulemerero wa chisomo chake, umene watipatsa kwaulere mwa Khristu amene amamukonda.

02 Aroma 8:1

Choncho, tsopano amene ali mwa Khristu Yesu alibe mlandu owatsutsa

03 Akolose 1:21-22

Kale inu munali kutali ndi Mulungu ndipo munali adani a Mulungu mʼmaganizo mwanu chifukwa cha khalidwe lanu loyipa. Koma tsopano Iye anakuyanjanitsani mʼthupi la Khristu kudzera mu imfa kuti akuperekeni pamaso pake oyera, opanda banga ndi opanda chotsutsidwa nacho

04 Aroma 15:7

Tsopano landiranani wina ndi mnzake, monganso Khristu anakulandirani inu, ndi cholinga choti Mulungu alemekezeke.

05 Yohane 6:37

Zonse zimene Atate andipatsa zidzabwera kwa Ine, ndipo aliyense amene adzabwera kwa Ine sindidzamutaya kunja.

06 Agalatiya 2:20

Ndinapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano mʼthupi lino, ndi moyo mwachikhulupiriro mwa Mwana wa Mulungu, amene anandikonda nadzipereka yekha chifukwa cha ine.

07 2 Akorinto 5:21

Chifukwa cha ife, Mulungu anasandutsa wopanda tchimoyo kukhala tchimo, kuti mwa Iye ife tikakhale chilungamo cha Mulungu.

08 1 Yohane 3:1

Taonani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate anatikonda nacho, kuti titchedwe ana a Mulungu! Ndipo nʼchimene ife tili! Nʼchifukwa chake dziko lapansi silitidziwa chifukwa silinamudziwe Iye.

09 Agalatiya 3:26

Nonse ndinu ana a Mulungu kudzera mʼchikhulupiriro mwa Khristu Yesu,

10 Aroma 8:15-16

Mzimu amene inu munalandira samakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha, koma Mzimu amakusandutsani ana. Ndipo mwa Iye ife timafuwula kuti, “Abba, Atate.” Mzimu mwini amavomerezana ndi mzimu wathu kuti ife ndife ana a Mulungu.

11 Yohane 1:12

Koma kwa onse amene anamulandira Iye, kwa amene anakhulupirira mʼdzina lake, Iye anawapatsa mphamvu yokhala ana a Mulungu;

12 Aefeso 2:13

Koma tsopano mwa Khristu Yesu, inu amene nthawi ina munali kutali, mwabweretsedwa pafupi kudzera mʼmagazi a Khristu.

13 Aroma 5:8

Koma Mulungu anaonetsa chikondi chake kwa ife chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu anatifera.

Mitu yofanana