Mavesi a m'Baibulo Onena za Kutaya Mtima

Mavesi 9 a m'Baibulo onena za Kutaya Mtima oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Masalimo 42:11

Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika chonchi mʼkati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamutamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.

02 2 Akorinto 4:8-9

Tapanikizika kwambiri mbali zonse koma osaphwanyika; tathedwa nzeru koma osataya mtima; tazunzidwa, koma osasiyidwa; takanthidwa, koma osawonongeka.

03 Masalimo 34:18

Yehova ali pafupi kwa osweka mtima ndipo amapulumutsa iwo amene asweka mu mzimu.

04 Maliro 3:21-23

Komabe ndimakumbukira zimenezi, nʼchifukwa chake ndili ndi chiyembekezo. Ife sitinawonongekeretu chifukwa chikondi cha Yehova ndi chachikulu, ndi chifundo chake ndi chosatha. Zimaoneka zatsopano mmawa uliwonse; kukhulupirika kwanu nʼkwakukulu.

05 Masalimo 40:1-2

Mofatsa ndinadikira Yehova Iye anatembenukira kwa ine ndipo anamva kulira kwanga. Ananditulutsa mʼdzenje lachitayiko, mʼthope ndi mʼchithaphwi; Iye anakhazikitsa mapazi anga pa thanthwe ndipo anandipatsa malo oyimapo olimba.

06 Masalimo 27:13-14

Ine ndikutsimikiza mtima za zimenezi; ndidzaona ubwino wa Yehova mʼdziko la anthu amoyo. Dikirani pa Yehova; khalani anyonga ndipo limbani mtima nimudikire Yehova.

07 Aroma 8:38-39

Pakuti ine ndatsimikiza ndi mtima wonse kuti ngakhale imfa, kapena moyo, ngakhale angelo, kapena ziwanda, ngakhale zinthu zilipo, kapena zili mʼtsogolo, kapena mphamvu zina, ngakhale kutalika, kapena kuya, kapena chilichonse mʼchilengedwe chonse, sizingathe kutisiyanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

08 Masalimo 73:26

Thupi ndi mtima wanga zitha kufowoka, koma Mulungu ndiye mphamvu ya mtima wanga ndi cholandira changa kwamuyaya.

09 Mika 7:8

Iwe mdani wanga, usandiseke! Ngakhale ndagwa, ndidzauka. Ngakhale ndikukhala mu mdima, Yehova ndiye kuwunika kwanga.

Mitu yofanana