Mavesi a m'Baibulo Onena za Kugonjetsa Tchimo
Mavesi 6 a m'Baibulo onena za Kugonjetsa Tchimo oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Tchimo silidzakhalanso ndi mphamvu pa inu, chifukwa Malamulo sakulamulira moyo wanu koma chisomo.
Palibe mayesero amene mwakumana nawo oposa amene anthu ena onse anakumana nawo. Mulungu ngokhulupirika; sadzalola kuti inu muyesedwe koposa muyeso umene mutha kupirira. Koma pamene mwayesedwa, Iyenso adzakupatsani njira yopambanira mayeserowo.
Koma tikavomereza machimo athu, Iye ndi wokhulupirika ndi wolungama ndipo adzatikhululukira machimo athu, nadzatiyeretsa ndi kutichotsera chosalungama chilichonse.
Pakuti ngati inu mukhala monga mwa khalidwe lauchimo, mudzafa. Koma ngati mwa Mzimu mupha ntchito zoyipa zathupi, mudzakhala ndi moyo.
Koma munthu aliyense amayesedwa akakokedwa ndi zilakolako zake zoyipa ndi kukopedwa nazo. Pamenepo, chilakolako chikakula chimabala tchimo; ndipo tchimo likakhwima limabereka imfa.
Koma tiyamike Mulungu amene amatipambanitsa mwa Ambuye athu Yesu Khristu.