Mavesi a m'Baibulo Onena za Manyazi

Mavesi 5 a m'Baibulo onena za Manyazi oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Aroma 10:11

Pakuti Malemba akuti, “Aliyense amene akhulupirira Iye, sadzachititsidwa manyazi.”

02 Yesaya 61:7

Chifukwa manyazi awo anali owirikiza; ndi kuti munalandira chitonzo ndi kutukwana, adzakondwera ndi cholowa chawo, tsono adzalandira cholowa chawo cha chigawo cha dziko mowirikiza, ndipo chimwemwe chamuyaya chidzakhala chawo.

03 Masalimo 34:5

Iwo amene amayangʼana kwa Iye, nkhope zawo zimanyezimira; nkhope zawo sizikhala zophimbidwa ndi manyazi.

04 Aroma 8:1

Choncho, tsopano amene ali mwa Khristu Yesu alibe mlandu owatsutsa

05 Yesaya 54:4

“Usachite mantha; sadzakunyozanso. Usakhumudwe; sudzapeputsidwanso. Udzayiwala za manyazi zimene zinakuchitikira nthawi ya unyamata wako ndipo za manyazi zimene zinakuchitikira pa nthawi ya umasiye wako sudzazikumbukanso.

Mitu yofanana