Mavesi a m'Baibulo Onena za Maganizo a Khristu

Mavesi 15 a m'Baibulo onena za Maganizo a Khristu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 1 Akorinto 2:16

Pakuti “Ndani anadziwa malingaliro a Ambuye, kuti akhoza kumulangiza Iye.” Koma tili nawo mtima wa Khristu.

02 Afilipi 2:5

Pa ubale wanu wina ndi mnzake, mukhale ndi mtima wofanana ndi wa Khristu Yesu:

03 Aroma 12:2

Musafanizidwenso ndi makhalidwe a dziko lino koma musandulike pokonzanso maganizo anu. Ndipo mudzadziwa ndi kuzindikira chifuniro chabwino cha Mulungu chomwe ndi chokondweretsa ndi changwiro.

04 1 Akorinto 2:12

Mzimu amene tinalandira ife si wa dziko lapansi koma Mzimu wochokera kwa Mulungu wotipatsa ife mwaulere.

05 Akolose 2:3

Mwa Iyeyu muli chuma chonse chobisidwa cha nzeru ndi chidziwitso.

06 Afilipi 2:6-8

Iyeyu, pokhala Mulungu ndithu, sanatenge kufanana ndi Mulungu kukhala chinthu choyenera kuchigwiritsa. Koma anadzichepetsa kotheratu nakhala ndi khalidwe ngati la kapolo ndi kukhala munthu ngati anthu ena onse. Ndipo pokhala munthu choncho anadzichepetsa yekha ndipo anamvera mpaka imfa yake, imfa yake ya pamtanda!

07 Yohane 15:15

Ine sindikutchulaninso antchito, chifukwa wantchito sadziwa zimene bwana wake akuchita. Mʼmalo mwake Ine ndakutchani abwenzi pakuti zilizonse zimene ndinaphunzira kwa Atate, Ine ndakudziwitsani.

08 Aefeso 4:23

kuti mukonzedwe mwatsopano mʼmitima mwanu;

09 Aroma 8:6

Kuyika mtima pa zathupi ndi imfa koma kuyika mtima pa za Mzimu ndi moyo ndi mtendere.

10 1 Akorinto 1:30

Nʼchifukwa cha Iye kuti inu muli mwa Khristu Yesu, amene wakhala nzeru ya kwa Mulungu, kwa ife, kunena kuti kulungama kwathu, chiyero ndi chipulumutso.

11 Yohane 8:29

Iye amene anandituma Ine ali nane pamodzi. Iye sanandisiye ndekha popeza nthawi zonse ndimachita zomwe zimamukondweretsa Iye.”

12 Ahebri 4:15

Pakuti sitili ndi Mkulu wa ansembe amene sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofowoka zathu. Koma tili naye amene anayesedwa mʼnjira zonse monga ife, koma sanachimwe.

13 Afilipi 2:3

Musachite kalikonse ndi mtima odzikonda chabe kapena odzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa ndipo aliyense aziona mnzake ngati womuposa iyeyo.

14 Yesaya 50:4

Ambuye Yehova anandiphunzitsa mawu oyenera kuyankhula kudziwa mawu olimbitsa mtima anthu ofowoka. Mmawa mulimonse amandidzutsa, amathwetsa khutu langa kuti ndimve monga amachitira munthu amene akuphunzira.

15 Yohane 5:30

Pakuti sindingathe kuchita kena kalikonse pa ndekha. Ine ndimaweruza molingana ndi zomwe Mulungu wandiwuza ndipo kuweruza kwanga ndi kolungama. Ine sindifuna kudzikondweretsa ndekha koma Iye amene anandituma.

Mitu yofanana