Masalimo 87

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (Biblica)

Iye wakhazikitsa maziko ake pa phiri loyera;

Yehova amakonda zipata za Ziyoni kupambana malo onse okhalamo a Yakobo.

Za ulemerero wako zimakambidwa, Iwe mzinda wa Mulungu: Sela

“Ndidzanena za Rahabe ndi Babuloni pakati pa iwo amene amandidziwa. Dzikonso la Filisitiya, Turo pamodzi ndi Kusi, ndipo ndidzati, ‘Uyu anabadwira mʼZiyoni.’ ”

Ndithudi, za Ziyoni adzanena kuti, “Uyu ndi uyo anabadwira mwa iye, ndipo Wammwambamwamba adzakhazikitsa iyeyo.”

Yehova adzalemba mʼbuku la kawundula wa anthu a mitundu ina: “Uyu anabadwira mʼZiyoni.” Sela

Oyimba ndi ovina omwe adzati, “Akasupe anga onse ali mwa iwe.”

Masalimo

Tsegulani chowerengera chogwirizana kusintha matembenuzidwe, kusintha malembedwe, ndi kulemba zizindikiro pa mavesi — kapena onani mavesi malinga ndi mutu.

© 2002, 2016 Biblica, Inc. · CC BY-SA 4.0