Masalimo 54

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (Biblica)

Pulumutseni Inu Mulungu, mwa dzina lanu; onetsani kuti ndine wosalakwa mwamphamvu yanu.

Imvani pemphero langa, Inu Mulungu mvetserani mawu a pakamwa panga.

Alendo akundithira nkhondo; anthu ankhanza akufunafuna moyo wanga, anthu amene salabadira za Mulungu.

Zoonadi Mulungu ndi thandizo langa; Ambuye ndiye amene amandichirikiza ine.

Lolani kuti choyipa chifike pa iwo amene amandichita chipongwe; mwa kukhulupirika kwanu awonongeni.

Ine ndidzapereka nsembe yaufulu kwa Inu; ndidzatamanda dzina lanu, Inu Yehova, pakuti ndi labwino.

Pakuti Iyeyo wandipulumutsa ku masautso anga onse, ndipo maso anga apenya kupambana kwa pa adani anga.

Masalimo

Tsegulani chowerengera chogwirizana kusintha matembenuzidwe, kusintha malembedwe, ndi kulemba zizindikiro pa mavesi — kapena onani mavesi malinga ndi mutu.

© 2002, 2016 Biblica, Inc. · CC BY-SA 4.0