Masalimo 120

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (Biblica)

1Ndimafuwulira kwa Yehova mʼmasautso anga, ndipo Iye amandiyankha.

2Pulumutseni Yehova ku milomo yabodza, ndi kwa anthu achinyengo.

3Kodi adzakuchitani chiyani, ndipo adzawonjezerapo zotani, inu anthu achinyengo?

4Adzakulangani ndi mivi yakuthwa ya munthu wankhondo, ndi makala oyaka a mtengo wa tsanya.

5Tsoka ine kuti ndimakhala ku Mesaki, kuti ndimakhala pakati pa matenti a ku Kedara!

6Kwa nthawi yayitali ndakhala pakati pa iwo amene amadana ndi mtendere.

7Ine ndine munthu wamtendere; koma ndikamayankhula, iwo amafuna nkhondo.

Masalimo

Open the interactive reader to switch translations, adjust type, and mark verses — or browse verses by topic.

© 2002, 2016 Biblica, Inc. · CC BY-SA 4.0