Masalimo 150

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (Biblica)

Tamandani Yehova. Tamandani Mulungu mʼmalo ake opatulika; mutamandeni ku thambo lake lamphamvu.

Mutamandeni chifukwa cha machitidwe ake amphamvu; mutamandeni chifukwa cha ukulu wake wopambana.

Mutamandeni poyimba malipenga, mutamandeni ndi pangwe ndi zeze.

Mutamandeni ndi matambolini ndi kuvina, mutamandeni ndi zingwe ndi zitoliro.

Mutamandeni ndi ziwaya zolira za malipenga, mutamandeni ndi ziwaya zolira kwambiri.

Chamoyo chilichonse chopuma chitamande Yehova. Tamandani Yehova.

Masalimo

Tsegulani chowerengera chogwirizana kusintha matembenuzidwe, kusintha malembedwe, ndi kulemba zizindikiro pa mavesi — kapena onani mavesi malinga ndi mutu.

© 2002, 2016 Biblica, Inc. · CC BY-SA 4.0