Masalimo 75
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (Biblica)
Tikuthokoza Inu Mulungu, tikuthokoza, pakuti dzina lanu lili pafupi nafe, anthutu amafotokoza za ntchito zanu zodabwitsa.
Mumati, “Ine ndimayika nthawi yoyenera, ndine amene ndimaweruza mwachilungamo.
Pamene dziko lapansi ndi anthu ake onse anjenjemera, ndine amene ndimagwiriziza mizati yake molimba. Sela
Kwa odzitama ndikuti, ‘Musadzitamenso,’ ndipo kwa oyipa, ‘Musatukulenso nyanga zanu.
Musatukule nyanga zanu motsutsana ndi kumwamba; musayankhule ndi khosi losololoka.’ ”
Kugamula milandu sikuchokera kummawa kapena kumadzulo kapena ku chipululu.
Koma ndi Mulungu amene amaweruza: Iyeyo amatsitsa wina, nakwezanso wina.
Mʼdzanja la Yehova muli chikho chodzaza ndi vinyo wochita thovu, wosakanizidwa ndi zokometsera; Iye amamutsanulira pansi ndipo onse oyipa a dziko lapansi amamwa ndi senga zake zonse.
Kunena za ine, ndidzalengeza izi kwamuyaya; ndidzayimba matamando kwa Mulungu wa Yakobo.
Ndidzadula nyanga za onse oyipa koma nyanga za olungama zidzakwezedwa.
Masalimo
- 1
- 2
- 3
- 4
- 5
- 6
- 7
- 8
- 9
- 10
- 11
- 12
- 13
- 14
- 15
- 16
- 17
- 18
- 19
- 20
- 21
- 22
- 23
- 24
- 25
- 26
- 27
- 28
- 29
- 30
- 31
- 32
- 33
- 34
- 35
- 36
- 37
- 38
- 39
- 40
- 41
- 42
- 43
- 44
- 45
- 46
- 47
- 48
- 49
- 50
- 51
- 52
- 53
- 54
- 55
- 56
- 57
- 58
- 59
- 60
- 61
- 62
- 63
- 64
- 65
- 66
- 67
- 68
- 69
- 70
- 71
- 72
- 73
- 74
- 75
- 76
- 77
- 78
- 79
- 80
- 81
- 82
- 83
- 84
- 85
- 86
- 87
- 88
- 89
- 90
- 91
- 92
- 93
- 94
- 95
- 96
- 97
- 98
- 99
- 100
- 101
- 102
- 103
- 104
- 105
- 106
- 107
- 108
- 109
- 110
- 111
- 112
- 113
- 114
- 115
- 116
- 117
- 118
- 119
- 120
- 121
- 122
- 123
- 124
- 125
- 126
- 127
- 128
- 129
- 130
- 131
- 132
- 133
- 134
- 135
- 136
- 137
- 138
- 139
- 140
- 141
- 142
- 143
- 144
- 145
- 146
- 147
- 148
- 149
- 150
Tsegulani chowerengera chogwirizana kusintha matembenuzidwe, kusintha malembedwe, ndi kulemba zizindikiro pa mavesi — kapena onani mavesi malinga ndi mutu.
© 2002, 2016 Biblica, Inc. · CC BY-SA 4.0