Masalimo 129

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (Biblica)

“Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga,” anene tsono Israeli;

“Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga, koma sanandipambane.

Anthu otipula analima pa msana panga ndipo anapangapo mizere yayitali:

Koma Yehova ndi wolungama; Iye wandimasula ku zingwe za anthu oyipa.”

Onse amene amadana ndi Ziyoni abwezedwe pambuyo mwamanyazi.

Akhale ngati udzu womera pa denga la nyumba, umene umafota usanakule;

sungadzaze manja a owumweta kapena manja a omanga mitolo.

Odutsa pafupi asanene kuti, “Dalitso la Yehova lili pa inu; tikukudalitsani mʼdzina la Yehova.”

Masalimo

Tsegulani chowerengera chogwirizana kusintha matembenuzidwe, kusintha malembedwe, ndi kulemba zizindikiro pa mavesi — kapena onani mavesi malinga ndi mutu.

© 2002, 2016 Biblica, Inc. · CC BY-SA 4.0