Masalimo 47

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (Biblica)

1Ombani mʼmanja, inu anthu onse; fuwulani kwa Mulungu ndi mawu achimwemwe.

2Ndi woopsadi Yehova Wammwambamwamba; Mfumu yayikulu ya dziko lonse lapansi!

3Iye anatigonjetsera mitundu yambirimbiri ya anthu; anayika anthu pansi pa mapazi athu.

4Iye anatisankhira cholowa chathu, chonyaditsa cha Yakobo, amene anamukonda. Sela

5Mulungu wakwera, anthu akumufuwulira mwachimwemwe, Yehova wakwera, akumuyimbira malipenga.

6Imbani matamando kwa Mulungu, imbani matamando; imbani matamando kwa mfumu yathu, imbani matamando.

7Pakuti Mulungu ndi mfumu ya dziko lonse lapansi; imbirani Iye salimo la matamando.

8Mulungu akulamulira mitundu ya anthu; Mulungu wakhala pa mpando wake waufumu woyera.

9Anthu otchuka mwa anthu a mitundu ina asonkhana monga anthu a Mulungu wa Abrahamu, pakuti mafumu a dziko lapansi ndi ake a Mulungu; Iye wakwezedwa kwakukulu.

Masalimo

Open the interactive reader to switch translations, adjust type, and mark verses — or browse verses by topic.

© 2002, 2016 Biblica, Inc. · CC BY-SA 4.0