Masalimo 112

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (Biblica)

Tamandani Yehova. Wodala munthu amene amaopa Yehova, amene amakondwera kwambiri ndi malamulo ake.

Ana ake adzakhala amphamvu mʼdziko; mʼbado wa olungama mtima udzadalitsidwa.

Kulemera ndi chuma zili mʼnyumba yake, ndipo chilungamo chake ndi chosatha.

Ngakhale mu mdima kuwala kumatulukira olungama mtima; wokoma mtima, wachifundo ndi wowongoka mtima.

Zinthu zabwino zidzabwera kwa iye amene amapereka mowolowamanja ndi wokongoletsa mwaufulu, amene amachita ntchito yake mwachilungamo.

Ndithu sadzagwedezeka; munthu wolungama sadzayiwalika mpaka muyaya.

Saopa akamva zoyipa zimene zachitika; mtima wake ndi wokhazikika ndipo amadalira Yehova.

Mtima wake ndi wotetezedwa, sadzakhala ndi mantha; potsiriza pake adzayangʼana adani ake mwachipambano.

Wopereka mphatso zake mowolowamanja kwa osauka, chilungamo chake chimanka mpaka muyaya; nyanga yake idzakwezedwa mwaulemu.

Munthu woyipa adzaona zimenezi ndipo adzapsa mtima; adzakukuta mano ake ndipo adzasungunuka. Zolakalaka za anthu oyipa sizidzachitika konse.

Masalimo

Tsegulani chowerengera chogwirizana kusintha matembenuzidwe, kusintha malembedwe, ndi kulemba zizindikiro pa mavesi — kapena onani mavesi malinga ndi mutu.

© 2002, 2016 Biblica, Inc. · CC BY-SA 4.0