Masalimo 6

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (Biblica)

Inu Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu, kapena kundilanga mu ukali wanu.

Ndichitireni chifundo Inu Yehova, pakuti ndalefuka; Inu Yehova chiritseni, pakuti mafupa anga ali pa ululu waukulu.

Moyo wanga uli pa mazunzo aakulu. Mpaka liti, Inu Yehova, mpaka liti?

Tembenukani Inu Yehova, ndipo mundilanditse; pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.

Palibe amene amakukumbukirani pamene wamwalira; Amakutamandani ndani ali ku manda?

Ine ndatopa ndi kubuwula; usiku wonse pa bedi panga pamadzaza ndi misozi yanga; ndimanyowetsa pogona panga ndi misozi.

Maso anga atupa chifukwa cha chisoni; akulephera kuona chifukwa cha adani anga.

Chokani kwa ine inu nonse amene mumachita zoyipa, pakuti Yehova wamva kulira kwanga.

Yehova wamva kupempha kwanga kofuna chifundo; Yehova walandira pemphero langa.

Adani anga onse adzachita manyazi ndipo adzakhala ndi mantha; adzabwerera msangamsanga mwa manyazi.

Masalimo

Tsegulani chowerengera chogwirizana kusintha matembenuzidwe, kusintha malembedwe, ndi kulemba zizindikiro pa mavesi — kapena onani mavesi malinga ndi mutu.

© 2002, 2016 Biblica, Inc. · CC BY-SA 4.0