Masalimo 113

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (Biblica)

Tamandani Yehova. Mutamandeni, inu atumiki a Yehova, tamandani dzina la Yehova.

Yehova atamandidwe, kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Kuyambira ku matulukiro a dzuwa mpaka ku malowero ake, dzina la Yehova liyenera kutamandidwa.

Yehova wakwezeka pa anthu a mitundu yonse, ulemerero wake ndi woposa mayiko akumwamba.

Ndani wofanana ndi Yehova Mulungu wathu, Iye amene amakhala mwaufumu mmwamba?

amene amawerama pansi kuyangʼana miyamba ndi dziko lapansi?

Iye amakweza munthu wosauka kuchoka pa fumbi ndi kutukula munthu wosowa kuchoka pa dzala;

amawakhazika pamodzi ndi mafumu, pamodzi ndi mafumu a anthu ake.

Amakhazikitsa mayi wosabereka mʼnyumba yake monga mayi wa ana wosangalala. Tamandani Yehova.

Masalimo

Tsegulani chowerengera chogwirizana kusintha matembenuzidwe, kusintha malembedwe, ndi kulemba zizindikiro pa mavesi — kapena onani mavesi malinga ndi mutu.

© 2002, 2016 Biblica, Inc. · CC BY-SA 4.0