Masalimo 12

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (Biblica)

1Thandizeni Yehova pakuti palibe munthu wokhulupirika; okhulupirika akusowa pakati pa anthu.

2Aliyense amanamiza mʼbale wake; ndi pakamwa pawo pabodza amayankhula zachinyengo.

3Inu Yehova tsekani milomo yonse yachinyengo ndi pakamwa paliponse podzikuza.

4Pakamwa pamene pamati, “Ife tidzapambana ndi kuyankhula kwathu; pakamwapa ndi pathupathu, tsono mbuye wathu ndani?”

5“Chifukwa cha kuponderezedwa kwa anthu opanda mphamvu ndi kubuwula kwa anthu osowa, Ine ndidzauka tsopano,” akutero Yehova, “Ndidzawateteza kwa owazunza.”

6Ndipo mawu a Yehova ndi angwiro monga siliva oyengedwa mʼngʼanjo yadothi, oyengedwa kasanu nʼkawiri.

7Inu Yehova mudzatitchinjiriza ndipo mudzatiteteza kwa anthu otere kwamuyaya.

8Oyipa amangoyendayenda ponseponse anthu akamayamikira zochita zawo.

Masalimo

Open the interactive reader to switch translations, adjust type, and mark verses — or browse verses by topic.

© 2002, 2016 Biblica, Inc. · CC BY-SA 4.0