Masalimo 149

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (Biblica)

1Tamandani Yehova. Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, matamando ake mu msonkhano wa oyera mtima.

2Israeli asangalale mwa mlengi wake; anthu a ku Ziyoni akondwere mwa Mfumu yawo.

3Atamande dzina lake povina ndi kuyimbira Iye nyimbo ndi tambolini ndi pangwe.

4Pakuti Yehova amakondwera ndi anthu ake; Iye amaveka chipulumutso odzichepetsa.

5Oyera mtima asangalale mu ulemu wake ndi kuyimba mwachimwemwe pa mabedi awo.

6Matamando a Mulungu akhale pakamwa pawo, ndi lupanga lakuthwa konsekonse mʼmanja mwawo,

7kubwezera chilango anthu a mitundu ina, ndi kulanga anthu a mitundu yonse,

8kumanga mafumu awo ndi zingwe, anthu awo otchuka ndi unyolo wachitsulo,

9kuchita zimene zinalembedwa zotsutsana nawo Uwu ndi ulemerero wa oyera mtima ake onse. Tamandani Yehova.

Masalimo

Open the interactive reader to switch translations, adjust type, and mark verses — or browse verses by topic.

© 2002, 2016 Biblica, Inc. · CC BY-SA 4.0