Mavesi a m'Baibulo Onena za Tayani Nkhawa Zanu
Mavesi 13 a m'Baibulo onena za Tayani Nkhawa Zanu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Tayani pa Iye nkhawa zanu zonse chifukwa ndiye amakusamalani.
Musade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa china chilichonse, mwa pemphero ndi chidandaulo pamodzi ndi chiyamiko, perekani zopempha zanu kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu, umene upambana nzeru zonse udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Tulani nkhawa zanu kwa Yehova ndipo Iye adzakulimbitsani; Iye sadzalola kuti wolungama agwe.
“Idzani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wodzichepetsa. Ndipo inu mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa ndi losavuta ndipo katundu wanga ndi wopepuka.”
Ndikachita mantha ndimadalira Inu.
Pereka njira yako kwa Yehova; dalira Iye ndipo Iyeyo adzachita izi:
“Nʼchifukwa chake ndikuwuzani kuti musadere nkhawa za moyo wanu kuti mudzadya chiyani kapena mudzamwa chiyani; kapenanso za thupi lanu kuti mudzavala chiyani. Kodi moyo suposa chakudya? Kodi thupi siliposa zovala?
Dalirani Iye nthawi zonse, inu anthu; khuthulani mitima yanu kwa Iye, pakuti Mulungu ndiye pothawirapo pathu. Sela
Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse ndipo usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa zochita zako zonse uvomereze kuti Mulungu alipo, ndipo Iye adzawongola njira zako.
Pamene nkhawa inakula mʼkati mwanga, chitonthozo chanu chinabweretsa chimwemwe mʼmoyo mwanga.
Inu mudzamupatsa munthu wa mtima wokhazikika mtendere weniweni.
Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni, iwe moyo wanga? Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga? Yembekezera Mulungu, pakuti ndidzamulambirabe, Mpulumutsi wanga ndi
Ine ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Ine sindikukupatsani monga dziko lapansi limaperekera. Mtima wanu usavutike ndipo musachite mantha.