Mavesi a m'Baibulo Onena za Wochirikizidwa
Mavesi 15 a m'Baibulo onena za Wochirikizidwa oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Tulani nkhawa zanu kwa Yehova ndipo Iye adzakulimbitsani; Iye sadzalola kuti wolungama agwe.
Tsono usaope, pakuti Ine ndili nawe; usataye mtima chifukwa Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu ndipo ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Zoonadi Mulungu ndi thandizo langa; Ambuye ndiye amene amandichirikiza ine.
Mpaka pamene mudzakalambe ndi kumera imvi ndidzakusamalirani ndithu. Ndinakulengani ndipo ndidzakunyamulani, ndidzakusamalirani ndi kukulanditsani.
Inu mumandipatsa chishango chachipambano, ndipo dzanja lanu lamanja limandichirikiza; mumawerama pansi kundikuza.
Ine ndimagona ndi kupeza tulo; ndimadzukanso chifukwa Yehova amandichirikiza.
koma iwo amene amakhulupirira Yehova adzalandira mphamvu zatsopano. Adzawuluka ngati chiwombankhanga; adzathamanga koma sadzalefuka, adzayenda koma sadzatopa konse.
Yehova amagwiriziza onse amene akugwa ndipo amakweza onse otsitsidwa.
Mulungu wamuyaya ndiye pothawirapo pathu, ndipo pa dziko lapansi amakusungani ndi mphamvu zosatha. Adzathamangitsa patsogolo panu mdani wanu, adzanena kuti, ‘Muwonongeni!’
ngakhale atapunthwa sadzagwa, pakuti Yehova amamutchinjiriza ndi dzanja lake.
Mundichirikize molingana ndi lonjezo lanu, ndipo ndidzakhala ndi moyo; musalole kuti chiyembekezo changa chipite pachabe.
Ife sitinawonongekeretu chifukwa chikondi cha Yehova ndi chachikulu, ndi chifundo chake ndi chosatha. Zimaoneka zatsopano mmawa uliwonse; kukhulupirika kwanu nʼkwakukulu.
Ndikanena kuti, “Phazi langa likuterereka,” chikondi chanu, Inu Yehova, chimandichirikiza.
Munawasunga zaka makumi anayi mʼchipululu ndipo sanasowe kanthu kalikonse. Zovala zawo sizinathe kapena mapazi awo kutupa.”
Sadzalola kuti phazi lako literereke; Iye amene amakusunga sadzawodzera.