Mavesi a m'Baibulo Onena za Chizunzo

Mavesi 10 a m'Baibulo onena za Chizunzo oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 2 Timoteyo 3:12

Kunena zoona, munthu aliyense amene akufuna kukhala moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi,

02 Mateyu 5:10-11

Odala ndi amene akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo, pakuti ufumu wakumwamba ndi wawo.” “Inu ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani, kukunenerani zoyipa zilizonse ndi kukunamizirani chifukwa cha Ine.

03 1 Petro 4:14

Ngati akuchitani chipongwe chifukwa cha dzina la Khristu, ndinu odala, ndiye kuti Mzimu waulemerero wa Mulungu uli pa inu.

04 Aroma 8:35-37

Ndani amene adzatilekanitsa ife ndi chikondi cha Khristu? Kodi ndi masautso, kapena zowawa, kapena mazunzo, kapena njala, kapena umaliseche, kapena choopsa, kapena lupanga? Monga kwalembedwa: “Chifukwa cha inu, ife tikuphedwa tsiku lonse: ife tikutengedwa ngati nkhosa zoti zikaphedwe.” Ayi, mu zonsezi ife ndife oposa agonjetsi mwa Iye amene anatikonda.

05 Yohane 15:20

Kumbukirani mawu amene ndinayankhula nanu akuti, ‘Palibe wantchito amene amaposa bwana wake.’ Ngati anandizunza Ine, iwo adzakuzunzaninso inu. Ngati anamvera chiphunzitso changa, iwo adzamvera chanunso.

06 2 Akorinto 4:8-9

Tapanikizika kwambiri mbali zonse koma osaphwanyika; tathedwa nzeru koma osataya mtima; tazunzidwa, koma osasiyidwa; takanthidwa, koma osawonongeka.

07 1 Petro 3:14

Koma ngakhale mumve zowawa chifukwa cha chilungamo, ndinu odala. “Musaope anthu, musachite mantha.”

Iwo anachoka ku Bwalo Lalikulu akukondwa chifukwa anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzina la Yesu.

09 Mateyu 5:44

Koma Ine ndikuwuzani kuti, ‘Kondani adani anu ndi kuwapempherera okuzunzani

10 2 Timoteyo 2:12

Ngati tinapirira, tidzalamuliranso naye pamodzi. Ngati ife timukana, Iye adzatikananso.

Mitu yofanana