Mavesi a m'Baibulo Onena za Mayesero, Masautso ndi Kuchiritsidwa
M'dziko lophwanyika, anthu a Mulungu sapulumutsidwa ku mayesero — koma sakhala okha mmenemo. Iye ali pafupi ndi osweka mtima, amachita zabwino kudzera m'masautso, ndi ndi mchiritsi wa thupi ndi moyo. Mavesi awa amabweretsa chitonthozo ndi chiyembekezo mu zowawa.
Ine ndiganiza kuti masautso amene tikuwamva nthawi ino, sakufanana ndi ulemerero umene udzaonetsedwa mwa ife.
Abale, muchiyese ngati chimwemwe chenicheni nthawi zonse pamene mukukumana ndi mayesero amitundumitundu. Inu mukudziwa kuti kuyesedwa kwa chikhulupiriro chanu kumabweretsa chipiriro.
Pakuti masautso athu ndi opepuka ndi a kanthawi, koma akutitengera ulemerero wamuyaya umene ndi wopambana kwambiri.
Inu Yehova, chiritseni, ndipo ndidzachira; pulumutseni ndipo ndidzapulumuka, chifukwa ndinu amene ndimakutamandani.
Kodi alipo wina mwa inu akudwala? Ayitane akulu ampingo kuti adzamupempherere ndi kumudzoza mafuta mʼdzina la Ambuye. Ndipo pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa munthu wodwalayo ndipo Ambuye adzamuutsa. Ngati wachimwa adzakhululukidwa.
Koma anandiwuza kuti, “Chisomo changa ndi chokukwanira, pakuti mphamvu zanga zimaoneka kwathunthu mwa munthu wofowoka.” Choncho ndidzadzitamandira mokondwera chifukwa cha zofowoka zanga, kuti mʼkutero mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.
Ngakhale ndiyende mʼchigwa cha mdima wakuda bii, sindidzaopa choyipa, pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditonthoza.
Tulani nkhawa zanu kwa Yehova ndipo Iye adzakulimbitsani; Iye sadzalola kuti wolungama agwe.
Kunena zoona, munthu aliyense amene akufuna kukhala moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi,
Abale, muchiyese ngati chimwemwe chenicheni nthawi zonse pamene mukukumana ndi mayesero amitundumitundu.
Mayeserowa abwera nʼcholinga chakuti chikhulupiriro chanu, chimene ndi chamtengo woposa wa golide, amene amawonongeka ngakhale amayengedwa ndi moto, chitsimikizike kuti ndi chenicheni. Pamenepo ndiye mudzalandire mayamiko, ulemerero ndi ulemu pamene Yesu Khristu adzaoneka.