Mavesi a m'Baibulo Onena za Oyengedwa ndi Moto

Mavesi 14 a m'Baibulo onena za Oyengedwa ndi Moto oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 1 Petro 1:7

Mayeserowa abwera nʼcholinga chakuti chikhulupiriro chanu, chimene ndi chamtengo woposa wa golide, amene amawonongeka ngakhale amayengedwa ndi moto, chitsimikizike kuti ndi chenicheni. Pamenepo ndiye mudzalandire mayamiko, ulemerero ndi ulemu pamene Yesu Khristu adzaoneka.

02 Zekariya 13:9

Chigawo chachitatuchi ndidzachiyika pa moto; ndidzawayeretsa monga momwe amayeretsera siliva ndi kuwayesa monga momwe amayesera golide. Adzayitana pa dzina langa ndipo Ine ndidzawayankha; Ine ndidzanena kuti, ‘Awa ndi anthu anga,’ ndipo iwo adzanena kuti, ‘Yehova ndiye Mulungu wathu.’ ”

03 Malaki 3:3

Iye adzachita kukhalira pansi ngati mmisiri woyenga ndi woyeretsa siliva. Iye adzayeretsa Alevi ndi kuwayenga ngati golide ndi siliva. Pamenepo Yehova adzakhala ndi anthu amene azidzabweretsa zopereka mwachilungamo,

04 Yobu 23:10

Koma Iye amadziwa mmene ndimayendera; Iyeyo akandiyesa adzandipeza kuti ndili ngati golide.

05 Yesaya 48:10

Taonani, ndinakuyeretsani ngati siliva; ndinakuyesani mʼngʼanjo yamasautso.

06 Miyambo 17:3

Siliva amamuyesa mʼngʼanjo ndipo golide amamuyesa mʼngʼanjo, koma Yehova amayesa mitima.

07 Masalimo 66:10

Pakuti Inu Mulungu munatiyesa; munatiyenga ngati siliva.

08 Yesaya 1:25

Ndidzatambasula dzanja langa kuti ndilimbane nawe; ndidzasungunula machimo ako nʼkuwachotsa, monga mmene amachotsera dzimbiri ndi mankhwala.

09 Danieli 12:10

Anthu ambiri adzayeretsedwa nakhala olungama wopanda chodetsa, koma oyipa adzakhala chiyipire. Palibe mmodzi wa anthu oyipa amene adzamvetsetsa koma okhawo amene ali anzeru adzamvetsetsa.

10 Yakobo 1:12

Wodala ndi munthu amene amapirira mʼmayesero, chifukwa akapambana adzalandira chipewa cha ulemerero chimene Mulungu analonjeza anthu amene amamukonda.

11 1 Akorinto 3:13

ntchito yake idzaonekera pamene Tsiku la chiweruzo lidzazionetsa poyera. Tsikulo lidzafika ndi moto, ndipo motowo ndi umene udzayesa ntchito ya munthu aliyense.

12 Yobu 42:5

Ndinkangomva za Inu ndi makutu anga, koma tsopanonso ndakuonani ndi maso anga.

13 Aroma 5:3-5

Koma si pokhapo ayi, koma ife tikukondweranso mʼmasautso athu chifukwa tikudziwa kuti masautso amatiphunzitsa kupirira. Ndipo kupirira kumabweretsa makhalidwe, makhalidwe amabweretsa chiyembekezo. Ndipo chiyembekezo chimenechi sichitikhumudwitsa chifukwa Mulungu mwa Mzimu Woyera, amene Iye anatipatsa, wadzaza mʼmitima mwathu ndi chikondi chake.

14 2 Akorinto 4:17

Pakuti masautso athu ndi opepuka ndi a kanthawi, koma akutitengera ulemerero wamuyaya umene ndi wopambana kwambiri.

Mitu yofanana