Mavesi a m'Baibulo Onena za Masautso

Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Masautso oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Aroma 8:18

Ine ndiganiza kuti masautso amene tikuwamva nthawi ino, sakufanana ndi ulemerero umene udzaonetsedwa mwa ife.

02 1 Petro 4:12-13

Abale okondedwa musadabwe ndi mayesero owawa amene mukukumana nawo ngati kuti china chake chachilendo chakuchitikirani. Koma kondwerani popeza mukumva zowawa pamodzi ndi Khristu, kuti mudzakondwere kwakukulu pamene ulemerero wake udzaonekera.

03 2 Akorinto 1:3-4

Alemekezeke Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, Atate achifundo chonse, Mulungu wachitonthozo chonse. Iye amatitonthoza ife mʼmavuto athu onse, kuti ifenso tithe kutonthoza amene ali pavuto lililonse ndi chitonthozo chimene ife tilandira kwa Mulungu.

04 Aroma 5:3-4

Koma si pokhapo ayi, koma ife tikukondweranso mʼmasautso athu chifukwa tikudziwa kuti masautso amatiphunzitsa kupirira. Ndipo kupirira kumabweretsa makhalidwe, makhalidwe amabweretsa chiyembekezo.

05 Afilipi 1:29

Pakuti inu mwapatsidwa mwayi osati ongokhulupirira Khristu kokha, koma wakumva zowawa mʼmalo mwa Khristu.

06 1 Petro 2:21

Munayitanidwa kudzachita zimenezi, chifukwa Khristu anamva zowawa chifukwa cha inu, anakusiyirani chitsanzo, kuti inu mutsatire mʼmapazi ake.

07 2 Akorinto 1:5

Pakuti monga momwe tili mʼmasautso pamodzi ndi Khristu, momwemonso Khristu amatitonthoza kwambiri.

08 Afilipi 3:10

Ine ndikufuna kudziwa Khristu, ndithu, kudziwa mphamvu zake za kuuka kwa akufa. Ndikufuna kuyanjana naye mʼmasautso ake, kufanana naye pa imfa yake

09 1 Petro 5:10

Ndipo Mulungu wachisomo chonse, amene anakuyitanani ku ulemerero wake wamuyaya mwa Khristu, mutamva zowawa pa kanthawi, adzakukonzaninso ndi kukulimbitsani pa maziko olimba.

10 Aroma 8:17

Tsono ngati tili ana ake, ndiye kuti ndife olowa mʼmalo a Mulungu ndi olowa mʼmalo pamodzi ndi Khristu. Ngati ife timva zowawa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.

11 2 Timoteyo 2:12

Ngati tinapirira, tidzalamuliranso naye pamodzi. Ngati ife timukana, Iye adzatikananso.

12 Ahebri 2:18

Popeza Iye mwini anamva zowawa pamene anayesedwa, Iyeyo angathe kuthandiza amene akuyesedwanso.

Mitu yofanana