Mavesi a m'Baibulo Onena za Matenda
Mavesi 7 a m'Baibulo onena za Matenda oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Kodi alipo wina mwa inu akudwala? Ayitane akulu ampingo kuti adzamupempherere ndi kumudzoza mafuta mʼdzina la Ambuye. Ndipo pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa munthu wodwalayo ndipo Ambuye adzamuutsa. Ngati wachimwa adzakhululukidwa.
Yehova adzamuthandiza pamene akudwala ndipo adzamuchiritsa pa bedi lake la matenda.
Itafika nthawi yamadzulo, anthu anabweretsa kwa Iye anthu ambiri ogwidwa ndi ziwanda ndipo anatulutsa ziwandazo ndi mawu okha, nachiritsa odwala onse. Uku kunali kukwaniritsa zimene ananena mneneri Yesaya kuti, “Iye anatenga zofowoka zathu, nanyamula nthenda zathu.”
Ndithudi, iye anamva zowawa mʼmalo mwa ife; ndipo anasautsidwa mʼmalo mwathu. Koma ife tinkaganiza kuti ndi Mulungu amene akumulanga, kumukantha ndi kumusautsa.
Tamanda Yehova, iwe moyo wanga, ndipo usayiwale zabwino zake zonse. Amene amakhululuka machimo ako onse ndi kuchiritsa nthenda zako zonse,
Zokhumba zanga zonse zili poonekera pamaso panu Ambuye, kusisima kwanga sikunabisike kwa Inu.
Yesu atamva zimenezi, anawawuza kuti, “Anthu amene ali bwino safuna singʼanga koma odwala. Ine sindinabwere kudzayitana olungama, koma ochimwa.”