Mavesi a m'Baibulo Onena za Kuchiritsidwa
Mavesi 13 a m'Baibulo onena za Kuchiritsidwa oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Inu Yehova, chiritseni, ndipo ndidzachira; pulumutseni ndipo ndidzapulumuka, chifukwa ndinu amene ndimakutamandani.
Tamanda Yehova, iwe moyo wanga, ndipo usayiwale zabwino zake zonse. Amene amakhululuka machimo ako onse ndi kuchiritsa nthenda zako zonse,
Koma iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, ndipo anamuzunza chifukwa cha zoyipa zathu; iye analangidwa kuti ife tikhale ndi mtendere, ndipo ndi mabala ake ife tinachiritsidwa.
Yehova anati, “Ngati inu mudzamvetsa bwino mawu anga, kuchita zolungama, kumvera malamulo anga ndi kusamalitsa zimene ndikukuwuzani ndiye kuti Ine sindidzayika pa inu matenda amene ndinayika pa anthu a ku Igupto popeza ndine Yehova amene ndimakuchiritsani.”
Akutsogolera anthu osweka mtima ndi kumanga mabala awo.
Inu Yehova Mulungu wanga ndinapempha kwa Inu thandizo ndipo Inu munandichiritsa.
Ndipo pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa munthu wodwalayo ndipo Ambuye adzamuutsa. Ngati wachimwa adzakhululukidwa.
Koma inu amene mumaopa dzina langa, dzuwa lachilungamo lidzakutulukirani lili ndi kuwala kokuchiritsani. Ndipo inu mudzatuluka ndi kulumphalumpha ngati ana angʼombe amene atulutsidwa mʼkhola.
Iye mwini anasenza machimo athu mʼthupi lake pa mtanda, kuti ife tife kutchimo ndi kukhala ndi moyo potsata chilungamo, ndipo ndi mabala ake munachiritsidwa.
Yehova adzamuthandiza pamene akudwala ndipo adzamuchiritsa pa bedi lake la matenda.
Yesu anayendayenda mu Galileya kuphunzitsa mʼmasunagoge awo, nalalikira Uthenga Wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa matenda onse pakati pa anthu.
Usamadzione ngati wa nzeru. Uziopa Yehova ndi kupewa zoyipa. Ukatero thupi lako lidzakhala la moyo wabwino ndi mafupa ako adzakhala olimba.
“Bwerani, tiyeni tibwerere kwa Yehova. Iye watikhadzula, koma adzatichiritsa. Iye wativulaza, koma adzamanga mabala athu.