Mavesi a m'Baibulo Onena za Masautso
Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Masautso oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Pakuti masautso athu ndi opepuka ndi a kanthawi, koma akutitengera ulemerero wamuyaya umene ndi wopambana kwambiri.
Munthu wolungama atha kukhala ndi mavuto ambiri, Koma Yehova amamulanditsa ku mavuto onsewo,
Ndipo ife tikudziwa kuti zinthu zonse zimathandizana kuwachitira ubwino amene amakonda Mulungu, amene anayitanidwa monga mwa cholinga chake.
Tapanikizika kwambiri mbali zonse koma osaphwanyika; tathedwa nzeru koma osataya mtima; tazunzidwa, koma osasiyidwa; takanthidwa, koma osawonongeka.
Ndi bwino kuti ndinasautsidwa kuti ndithe kuphunzira malamulo anu.
Chitonthozo changa pa masautso anga ndi ichi: lonjezo lanu limasunga moyo wanga.
Yehova ali pafupi kwa osweka mtima ndipo amapulumutsa iwo amene asweka mu mzimu.
Yehova ndiye kothawirako kwa opsinjika mtima, linga pa nthawi ya mavuto.
Ndisanayambe kuzunzika ndinasochera, koma tsopano ndimamvera mawu anu.
Ngakhale amabweretsa zowawa, Iye adzawachitira chifundo, chifukwa chikondi chake ndi chosatha. Pakuti sabweretsa masautso mwadala, kapena zowawa kwa ana a anthu.
“Wodala munthu amene Mulungu amamudzudzula; nʼchifukwa chake usanyoze chilango cha Wamphamvuzonse.
Yehova ndi wabwino, ndiye kothawirako nthawi ya masautso. Amasamalira amene amamudalira,