Mavesi a m'Baibulo Onena za Chigwa
Mavesi 6 a m'Baibulo onena za Chigwa oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Ngakhale ndiyende mʼchigwa cha mdima wakuda bii, sindidzaopa choyipa, pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditonthoza.
Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu. Amandigoneka pa msipu wobiriwira, amanditsogolera ku madzi akumwa abwino, amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera mʼnjira zachilungamo chifukwa cha dzina lake.
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe; ndipo pamene ukuwoloka mitsinje, sidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto, sudzapsa; lawi la moto silidzakutentha.
Mulungu ndiye kothawira kwathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu pa nthawi ya mavuto. Nʼchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisunthike, ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja,
Pamene akudutsa chigwa cha Baka, amachisandutsa malo a akasupe; mvula ya chizimalupsa imadzazanso mayiwe ake.
Mumandikonzera chakudya adani anga akuona. Mumadzoza mutu wanga ndi mafuta; chikho changa chimasefukira.