Mavesi a m'Baibulo Onena za Mzimu Woyera
Mzimu ndi Mulungu mwini wokhala ndi anthu ake ndi mkati mwa anthu ake — Mthandizi wathu, Womtonthoza wathu, chizindikiro cha kuwomboledwa kwathu. Iye akukhuthulira chikondi cha Mulungu m'mitima yathu, akukulitsa zipatso zake m'miyoyo yathu, ndi kupereka mphatso zothandiza mpingo. Mavesi awa akukuthandiza kulandira Mzimu ndi kuyenda mogwirizana naye.
Mzimu Woyera
Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamutumiza mʼdzina langa adzakuphunzitsani zinthu zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndinakuwuzani.
Musaledzere ndi vinyo, chifukwa adzawononga moyo wanu. Mʼmalo mwake, mudzazidwe ndi Mzimu Woyera.
Popeza timakhala ndi moyo mwa Mzimu Woyera, tiyeni tiyende pamodzi ndi Mzimu Woyera.
Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthawi zonse.
Iye akabwera, adzatsutsa dziko lapansi za uchimo, zachilungamo ndi zachiweruzo.
Onse amene amatsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu ndi ana a Mulungu.
Koma pamene Iye, Mzimu wachoonadi, abwera, adzakutsogolerani mʼchoonadi chonse. Iye sadzayankhula mwa Iye yekha, adzayankhula zokhazo zimene wamva ndipo Iye adzakuwuzani zimene zikubwera.
Kodi inu simukudziwa kuti ndinu Nyumba ya Mulungu ndipo kuti Mzimu wa Mulungu amakhala mwa inu?
Momwemonso, Mzimu amatithandiza ife mʼkufowoka kwathu. Ife sitidziwa momwe tiyenera kupempherera koma Mzimu mwini amatipempherera mobuwula ndi mawu osafotokozedwa.
Malemba kuti ‘Aliyense amene akhulupirira Ine, mitsinje yamadzi amoyo idzatuluka kuchokera mʼkati mwake.’ ”
Ndipo inunso pamene munamva mawu a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, munayikidwanso mwa Khristu. Mutakhulupirira, anakusindikizani chizindikiro pokupatsani Mzimu Woyera amene Iye analonjeza.
Koma mudzalandira mphamvu Mzimu Woyera akadzafika pa inu; ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”
Chipatso ndi Mphatso za Mzimu
Koma chipatso cha Mzimu Woyera ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndi kudziretsa. Palibe lamulo loletsa zimenezi.
Pakuti Mzimu amene Mulungu anatipatsa, si Mzimu wotipatsa manyazi, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzisunga.
Aliyense agwiritse ntchito mokhulupirika mphatso iliyonse imene anayilandira potumikira ena ngati adindo ogwiritsa bwino ntchito mphatso za Mulungu za mitundumitundu.
Koma za inu, kudzoza kumene munalandira kwa Khristu kuli mwa inu, ndipo sipafunika wina aliyense kuti akuphunzitseni. Koma kudzozako kumakuphunzitsani zinthu zonse, ndipo popeza kudzoza kwakeko nʼkoona osati konama, monga munaphunzira, khalani mwa Iyeyo.
Ndipo tsopano zatsala zinthu zitatu: chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma chachikulu pa zonsezi ndi chikondi.
Funafunani chikondi, ndikufunitsitsa mphatso zauzimu, makamaka mphatso ya uneneri.
Nʼchifukwa chake ndikukukumbutsa kuti upemerere monga amachitira moto, mphatso imene Mulungu anakupatsa nditakusanjika manja.
Thupi ndi limodzi, ngakhale kuti lapangidwa ndi ziwalo zambiri. Ndipo ngakhale ziwalo zake zonse ndi zambiri, zimapanga thupi limodzi. Momwemonso ndi mmene alili Khristu.