Mavesi a m'Baibulo Onena za Mzimu Umathandiza Kufooka Kwathu

Mavesi 14 a m'Baibulo onena za Mzimu Umathandiza Kufooka Kwathu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Aroma 8:26

Momwemonso, Mzimu amatithandiza ife mʼkufowoka kwathu. Ife sitidziwa momwe tiyenera kupempherera koma Mzimu mwini amatipempherera mobuwula ndi mawu osafotokozedwa.

02 Aroma 8:27

Koma Iye amene amasanthula mitima yathu amadziwa maganizo a Mzimu, chifukwa Mzimu amapempherera oyera mtima molingana ndi chifuniro cha Mulungu.

03 Yohane 14:16

Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthawi zonse.

04 2 Akorinto 12:9

Koma anandiwuza kuti, “Chisomo changa ndi chokukwanira, pakuti mphamvu zanga zimaoneka kwathunthu mwa munthu wofowoka.” Choncho ndidzadzitamandira mokondwera chifukwa cha zofowoka zanga, kuti mʼkutero mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.

05 Afilipi 4:13

Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu.

06 Yesaya 40:31

koma iwo amene amakhulupirira Yehova adzalandira mphamvu zatsopano. Adzawuluka ngati chiwombankhanga; adzathamanga koma sadzalefuka, adzayenda koma sadzatopa konse.

07 Zekariya 4:6

Choncho iye anandiwuza kuti, “Mawu a Yehova kwa Zerubabeli ndi awa: ‘Osati mwa nkhondo kapena ndi mphamvu, koma ndi Mzimu wanga,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.

08 Masalimo 73:26

Thupi ndi mtima wanga zitha kufowoka, koma Mulungu ndiye mphamvu ya mtima wanga ndi cholandira changa kwamuyaya.

09 Aefeso 3:16

Ndikupemphera kuti kuchokera mʼchuma cha ulemerero wake alimbikitse moyo wanu wa mʼkati ndi mphamvu za Mzimu wake,

10 2 Akorinto 4:16

Nʼchifukwa chake ife sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifowokerafowokera, koma mʼkatimu tikulimbikitsidwa mwatsopano tsiku ndi tsiku.

11 Yesaya 41:10

Tsono usaope, pakuti Ine ndili nawe; usataye mtima chifukwa Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu ndipo ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

12 Masalimo 46:1

Mulungu ndiye kothawira kwathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu pa nthawi ya mavuto.

13 Yohane 14:26

Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamutumiza mʼdzina langa adzakuphunzitsani zinthu zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndinakuwuzani.

14 Aroma 15:13

Mulungu amene amatipatsa chiyembekezo adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pamene mukumudalira Iye, kuti chiyembekezo chanu chisefukire mwamphamvu ya Mzimu Woyera.

Mitu yofanana