Mavesi a m'Baibulo Onena za Kutsutsa kwa Mzimu
Mavesi 10 a m'Baibulo onena za Kutsutsa kwa Mzimu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Iye akabwera, adzatsutsa dziko lapansi za uchimo, zachilungamo ndi zachiweruzo.
Za uchimo, chifukwa anthu sakhulupirira Ine. Za chilungamo, chifukwa Ine ndi kupita kwa Atate, kumene simudzandionanso. Za chiweruzo, chifukwa wolamulira dziko lino lapansi waweruzidwa tsopano.
Koma pamene Iye, Mzimu wachoonadi, abwera, adzakutsogolerani mʼchoonadi chonse. Iye sadzayankhula mwa Iye yekha, adzayankhula zokhazo zimene wamva ndipo Iye adzakuwuzani zimene zikubwera.
Iye anatipulumutsa, osati chifukwa cha ntchito zathu zolungama zimene tinachita koma chifukwa cha chifundo chake. Anatipulumutsa potisambitsa, kutibadwitsa kwatsopano ndi kutikonzanso mwa Mzimu Woyera
Anthu atamva zimenezi, anatsutsika kwambiri mu mtima ndipo anati kwa Petro ndi atumwi enawo, “Abale, kodi ife tichite chiyani?”
Paulo atayankhula za chilungamo, za kudziretsa ndiponso za chiweruzo chimene chikubwera, Felike anachita mantha ndipo anati, “Basi tsopano! Pita. Tidzakuyitanitsa tikadzapeza mpata.”
Ntchito zawo zimaonetsa kuti Malamulowo alembedwa mʼmitima mwawo. Chikumbumtima chawonso chimawachitira umboni pakuti maganizo awo amawatsutsa kapena kuwavomereza.
Paja Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amalowa mpaka molumikizirana moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana fundo ndi mafuta a mʼmafupa. Amaweruza malingaliro ndi zokhumba za mʼmitima.
Iwo atamva izi anayamba kuchoka mmodzimmodzi, akuluakulu poyamba, mpaka Yesu anatsala yekha ndi mkaziyo atayimirira pomwepo.
chifukwa uthenga wathu wabwino sunafike kwa inu ndi mawu okha, koma ndi mphamvu za Mzimu Woyera ndi chitsimikizo chachikulu. Mukudziwa mmene tinkakhalira pakati panu kuti tikuthandizeni.