Mavesi a m'Baibulo Onena za Kuyenda Mwa Mzimu

Mavesi 10 a m'Baibulo onena za Kuyenda Mwa Mzimu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Agalatiya 5:25

Popeza timakhala ndi moyo mwa Mzimu Woyera, tiyeni tiyende pamodzi ndi Mzimu Woyera.

02 Agalatiya 5:16

Choncho ine ndikuti, mulole kuti Mzimu akutsogolereni ndipo simudzachita zofuna za thupi lanu la uchimo.

03 Aroma 8:4

ndi cholinga chakuti chilungamo chofunikira cha lamulo chikwaniritsidwe kwathunthu mwa ife amene sitikhala monga mwachikhalidwe chathu cha uchimo koma mwa Mzimu.

04 Agalatiya 5:22-23

Koma chipatso cha Mzimu Woyera ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndi kudziretsa. Palibe lamulo loletsa zimenezi.

05 Aroma 8:1

Choncho, tsopano amene ali mwa Khristu Yesu alibe mlandu owatsutsa

06 Aroma 8:5

Pakuti anthu amene amakhala monga mwa makhalidwe oyipa a thupi amayika malingaliro awo pa zinthu zathupi. Koma amene amakhala monga mwa Mzimu amayika malingaliro awo pa zinthu za Mzimu.

07 Aroma 8:13-14

Pakuti ngati inu mukhala monga mwa khalidwe lauchimo, mudzafa. Koma ngati mwa Mzimu mupha ntchito zoyipa zathupi, mudzakhala ndi moyo. Onse amene amatsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu ndi ana a Mulungu.

08 Agalatiya 5:18

Koma ngati Mzimu akutsogolerani, ndiye kuti simuli pansi pa lamulo.

09 Agalatiya 6:8

Pakuti amene amafesa zokondweretsa thupi lake la uchimo, kuchokera ku khalidwe limenelo adzakolola chiwonongeko; amene amafesa zokondweretsa Mzimu, kuchokera kwa Mzimu adzakolola moyo wosatha.

10 Aefeso 5:8-9

Pajatu inu nthawi ina munali mdima, koma tsopano ndinu kuwunika mwa Ambuye. Mukhale ngati ana akuwunika (pakuti pamene pali kuwunika pamapezekaponso zabwino zonse, chilungamo ndi choonadi).

Mitu yofanana