Mavesi a m'Baibulo Onena za Mphatso Zambiri, Mzimu Umodzi

Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Mphatso Zambiri, Mzimu Umodzi oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 1 Akorinto 12:4

Pali mphatso zosiyanasiyana, koma Mzimu yemweyo.

02 1 Akorinto 12:5-6

Pali mautumiki osiyanasiyana koma Ambuye yemweyo. Pali magwiridwe antchito osiyanasiyana, koma Mulungu yemweyo amagwira ntchito monsemo mwa anthu onse.

03 1 Akorinto 12:11

Zonsezi ndi ntchito za Mzimu mmodzi yemweyo, ndipo amapereka kwa munthu aliyense monga momwe Mzimuyo wafunira.

04 Aefeso 4:4

Pali thupi limodzi ndiponso Mzimu mmodzi, monganso pali chiyembekezo chimodzi chimene anakuyitanirani.

05 Aroma 12:5

Momwemonso mwa Khristu ife amene tili ambiri tipanga thupi limodzi ndipo chiwalo chilichonse ndi cholumikizika ku chinzake.

06 1 Akorinto 12:7

Tsono Mzimu amapereka mphatso kwa aliyense kuti ipindulire onse.

07 Aefeso 4:7

Koma aliyense wa ife wapatsidwa chisomo molingana ndi muyeso wa mphatso ya Khristu.

08 1 Akorinto 12:14

Tsopano thupi silinapangidwe ndi chiwalo chimodzi koma ndi ziwalo zambiri.

09 Aroma 12:6

Ife tili ndi mphatso zosiyana, molingana ndi chisomo chopatsidwa kwa ife. Ngati mphatso ya munthu ndi kunenera, musiyeni ayigwiritse ntchito molingana ndi chikhulupiriro chake.

10 Aefeso 4:11

Iye ndiye amene anapereka mphatso kwa ena kuti akhale atumwi ndi ena aneneri, ena alaliki, ndi ena abusa ndi aphunzitsi.

11 1 Akorinto 12:18

Koma zoona nʼzakuti, Mulungu anayika ziwalo mʼthupi, chilichonse monga momwe Iye anafunira.

Mitu yofanana