Mavesi a m'Baibulo Onena za Mphamvu Yauzimu
Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Mphamvu Yauzimu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Pakuti Mzimu amene Mulungu anatipatsa, si Mzimu wotipatsa manyazi, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzisunga.
Ndikupemphera kuti kuchokera mʼchuma cha ulemerero wake alimbikitse moyo wanu wa mʼkati ndi mphamvu za Mzimu wake,
Koma mudzalandira mphamvu Mzimu Woyera akadzafika pa inu; ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”
Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye ndi mwa mphamvu zake zazikulu.
Timapempheranso kuti Mulungu akulimbikitseni ndi mphamvu yake yonse ya ulemerero wake, kuti muzipirira zonse ndi mitima yofatsa ndi ya chimwemwe
Uthenga ndi ulaliki wanga sunali wa mawu anzeru ndi onyengerera koma woonetsa mphamvu za Mzimu, kuti chikhulupiriro chanu chisatsamire pa nzeru ya anthu koma pa mphamvu za Mulungu.
Mulungu amene amatipatsa chiyembekezo adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pamene mukumudalira Iye, kuti chiyembekezo chanu chisefukire mwamphamvu ya Mzimu Woyera.
Tsopano kwa Iye amene angathe kuchita zochuluka kuposa zimene tingapemphe, kapena kuganiza molingana ndi mphamvu zake zimene zikugwira ntchito mwa ife,