Mavesi a m'Baibulo Onena za Chipatso cha Mzimu
Mavesi 15 a m'Baibulo onena za Chipatso cha Mzimu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Koma chipatso cha Mzimu Woyera ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndi kudziretsa. Palibe lamulo loletsa zimenezi.
“Ine ndine mpesa; inu ndinu nthambi zake. Ngati munthu akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye, adzabereka zipatso zambiri; popanda Ine simungathe kuchita kanthu.
Chimodzimodzinso mtengo wabwino umabala chipatso chabwino, koma mtengo woyipa umabala chipatso choyipa.
Popeza timakhala ndi moyo mwa Mzimu Woyera, tiyeni tiyende pamodzi ndi Mzimu Woyera.
Ndipo tikupempherera zimenezi ndi cholinga chakuti inu mukhale moyo oyenera Ambuye ndi kumukondweretsa mʼnjira zonse. Kubereka chipatso pa ntchito iliyonse yabwino, ndi kukula mʼchidziwitso cha Mulungu.
Atate anga amalemekezedwa mukamabereka zipatso zochuluka, ndipo potero mudzionetsa kuti ndinu ophunzira anga.
Momwemonso, ndi zipatso zawo iwo mudzawazindikira.
Ndipo moyo wanu udzakhala odzazidwa ndi chipatso cha chilungamo chimene chimachokera mwa Yesu Khristu. Pakuti zimenezi zidzapereka ulemerero ndi matamando kwa Mulungu.
Koma nzeru imene imachoka kumwamba, poyamba ndi yangwiro, ndi yokonda mtendere, yoganizira za ena, yogonjera, yodzaza ndi chifundo ndi chipatso chabwino, yosakondera ndi yoona mtima.
(pakuti pamene pali kuwunika pamapezekaponso zabwino zonse, chilungamo ndi choonadi).
Koma tsopano pakuti inu mwamasulidwa ku tchimo ndipo mwasanduka akapolo a Mulungu, phindu lomwe mulipeza ndi kuyera mtima ndipo chotsatira chake ndi moyo wosatha.
Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani kuti mupite ndi kukabereka zipatso, zipatso zake za nthawi yayitali. Choncho Atate adzakupatsani chilichonse chimene mudzapempha mʼdzina langa.
Palibe chilango chimene chimaoneka kuti ndi chabwino pa nthawiyo, komatu chowawa. Koma pambuyo pake, chimabweretsa chipatso chachilungamo ndi mtendere kwa iwo amene aleredwa mwa njira imeneyi.
Iye ali ngati mtengo wodzalidwa mʼmbali mwa mitsinje ya madzi, umene umabereka zipatso zake pa nyengo yake ndipo masamba ake safota. Chilichonse chimene amachita amapindula nacho.
umene unafika kwa inu. Pa dziko lonse lapansi Uthenga Wabwino ukubereka chipatso ndi kukula monga momwe zakhala zikuchitikira pakati panu kuyambira tsiku limene munawumva ndi kuzindikira chisomo cha Mulungu mu choonadi chonse.