Mavesi a m'Baibulo Onena za Mphatso za Mzimu
Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Mphatso za Mzimu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Tsono Mzimu amapereka mphatso kwa aliyense kuti ipindulire onse.
Zonsezi ndi ntchito za Mzimu mmodzi yemweyo, ndipo amapereka kwa munthu aliyense monga momwe Mzimuyo wafunira.
Ife tili ndi mphatso zosiyana, molingana ndi chisomo chopatsidwa kwa ife. Ngati mphatso ya munthu ndi kunenera, musiyeni ayigwiritse ntchito molingana ndi chikhulupiriro chake.
Mzimu amapereka kwa munthu wina mawu anzeru, Mzimu yemweyonso amapereka kwa wina mawu achidziwitso. Kwa wina, Mzimu yemweyo amapereka chikhulupiriro, kwa wina mphatso zamachiritso, Mzimu yemweyo. Kwa wina mphamvu zochita zodabwitsa, kwa wina mawu a uneneri, kwa wina mphatso yozindikira mizimu, kwa wina malilime osiyanasiyana, ndiponso kwa wina kutanthauzira malilimewo.
Iye ndiye amene anapereka mphatso kwa ena kuti akhale atumwi ndi ena aneneri, ena alaliki, ndi ena abusa ndi aphunzitsi. Ntchito yawo ndi kukonza oyera mtima kuti agwire ntchito ya utumiki kuti thupi la Khristu lilimbikitsidwe.
Ndipo Mulungu mu mpingo anayika poyamba atumwi, kachiwiri aneneri, kachitatu aphunzitsi, kenaka ochita zozizwitsa, ena a mphatso zamachiritso, ena a mphatso yothandiza anzawo, ena a mphatso yotsogolera ndiponso ena a mphatso ya malilime.
Aliyense agwiritse ntchito mokhulupirika mphatso iliyonse imene anayilandira potumikira ena ngati adindo ogwiritsa bwino ntchito mphatso za Mulungu za mitundumitundu.
Ife tili ndi mphatso zosiyana, molingana ndi chisomo chopatsidwa kwa ife. Ngati mphatso ya munthu ndi kunenera, musiyeni ayigwiritse ntchito molingana ndi chikhulupiriro chake. Ngati ndi kutumikira, musiyeni atumikire. Ngati ndi kuphunzitsa, musiyeni aphunzitse. Ngati ndi kulimbikitsa, musiyeni alimbikitse. Ngati ndi kupereka kuthandiza osowa, musiyeni apereke mowolowamanja. Ngati ndi utsogoleri, musiyeni alamulire mosamala. Ngati ndi kuonetsa chifundo, musiyeni achite mosangalala.
Funafunani chikondi, ndikufunitsitsa mphatso zauzimu, makamaka mphatso ya uneneri.
Mulungu anachitiranso umboni pochita zizindikiro, zinthu zodabwitsa ndi zamphamvu zamitundumitundu ndi powapatsa mphatso za Mzimu Woyera monga mwachifuniro chake.
Koma aliyense wa ife wapatsidwa chisomo molingana ndi muyeso wa mphatso ya Khristu.
Koma zoona nʼzakuti, Mulungu anayika ziwalo mʼthupi, chilichonse monga momwe Iye anafunira.