Mavesi a m'Baibulo Onena za Kudziletsa

Mavesi 14 a m'Baibulo onena za Kudziletsa oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Agalatiya 5:23

kufatsa ndi kudziretsa. Palibe lamulo loletsa zimenezi.

02 Miyambo 25:28

Munthu amene samatha kudziretsa ali ngati mzinda umene adani awuthyola ndi kuwusiya wopanda malinga.

03 1 Akorinto 9:25

Aliyense wochita mpikisano amakonzekera mwamphamvu. Amachita izi kuti alandire mphotho yankhata yamaluwa yomwe imafota. Koma ife timachita izi kuti tilandire mphotho yosafota.

04 Tito 2:12

Chisomo chimatiphunzitsa kukana moyo osalemekeza Mulungu komanso zilakolako za dziko lapansi. Ndipo chimatiphunzitsa kukhala moyo odziletsa, olungama ndi opembedza Mulungu nthawi ino,

05 2 Petro 1:6

Pa nzeru muwonjezerepo kudziretsa, pa kudziretsa muwonjezerepo chipiriro, ndipo pa chipiriro muwonjezerepo khalidwe lolemekeza Mulungu.

06 Miyambo 16:32

Munthu wosapsa mtima msanga amaposa munthu wankhondo, munthu wowugwira mtima wake amaposa amene amalanda mzinda.

07 2 Timoteyo 1:7

Pakuti Mzimu amene Mulungu anatipatsa, si Mzimu wotipatsa manyazi, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzisunga.

08 1 Akorinto 9:27

Ine ndimazunza thupi langa ndi kulisandutsa kapolo kuti nditatha kulalikira ena, ineyo ndingadzapezeke wosayenera kulandira nawo mphotho.

09 Yakobo 1:19

Abale anga okondedwa, gwiritsitsani mawu awa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma asamafulumire kuyankhula, ndipo asamafulumirenso kupsa mtima.

10 Agalatiya 5:24

Amene ali ake a Khristu Yesu anapachika pa mtanda thupi lawo la uchimo pamodzi ndi zokhumba zawo ndi zolakalaka zawo.

11 1 Petro 5:8

Khalani odziretsa ndi atcheru. Mdani wanu mdierekezi amayendayenda monga mkango wobangula kufunafuna wina kuti amumeze.

12 Miyambo 29:11

Munthu wopusa amaonetsa mkwiyo wake, koma munthu wanzeru amadzigwira.

13 1 Atesalonika 5:6

Chomwecho tsono, tisafanane ndi ena amene akugona koma tikhale maso ndi odzisunga.

14 Aroma 13:14

Koma valani Ambuye Yesu Khristu ndipo musaganizire za momwe mungakwaniritsire zokhumba zachikhalidwe cha uchimo.

Mitu yofanana