Mavesi a m'Baibulo Onena za Kudzozedwa

Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Kudzozedwa oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 1 Yohane 2:27

Koma za inu, kudzoza kumene munalandira kwa Khristu kuli mwa inu, ndipo sipafunika wina aliyense kuti akuphunzitseni. Koma kudzozako kumakuphunzitsani zinthu zonse, ndipo popeza kudzoza kwakeko nʼkoona osati konama, monga munaphunzira, khalani mwa Iyeyo.

02 1 Yohane 2:20

Koma inu muli ndi kudzoza kochokera kwa Woyerayo, ndipo nonsenu mukudziwa choonadi.

03 2 Akorinto 1:21

Tsono ndi Mulungu amene anachititsa kuti inu ndi ife tiyime molimba mwa Khristu. Anatidzoza ife,

kuti Mulungu, anamudzoza Yesu, wa ku Nazareti ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu ndiponso mmene Iye anapita nachita zabwino ndi kuchiritsa onse amene anali pansi pa mphamvu ya mdierekezi, popeza kuti Mulungu anali naye.

05 Masalimo 23:5

Mumandikonzera chakudya adani anga akuona. Mumadzoza mutu wanga ndi mafuta; chikho changa chimasefukira.

06 Luka 4:18

“Mzimu wa Ambuye ali pa Ine; chifukwa wandidzoza kuti ndilalikire Uthenga Wabwino kwa osauka. Wandituma kuti ndilalikire kwa a mʼndende kuti amasulidwe ndi kwa osaona kuti apenyenso, kumasulidwa kwa osautsidwa,

07 Yesaya 61:1

Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine, chifukwa Yehova wandidzoza kuti ndilalikire uthenga wabwino kwa anthu osauka. Wandituma kuti ndikatonthoze anthu osweka mtima, ndikalengeze kwa akapolo kuti alandire ufulu ndiponso kuti ndikamasule a mʼndende.

08 1 Samueli 16:13

Samueli anatenga botolo la mafuta ndi kumudzoza pamaso pa abale ake, ndipo Mzimu wa Yehova unabwera mwamphamvu pa Davide kuyambira tsiku limenelo mpaka mʼtsogolo. Pambuyo pake Samueli anabwerera ku Rama.

Mitu yofanana