Mavesi a m'Baibulo Onena za Musazimitse Mzimu
Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Musazimitse Mzimu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Musazimitse moto wa Mzimu Woyera.
Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu amene mwasindikizidwa naye chizindikiro cha tsiku la kuwomboledwa.
Musanyoze mawu a uneneri. Yesani zinthu zonse. Gwiritsitsani chimene ndi chabwino.
“Anthu wokanika inu, osachita mdulidwe wa mu mtima ndi a makutu ogontha! Inu ofanana ndi makolo anu. Nthawi zonse mumakana kumvera Mzimu Woyera:
Popeza timakhala ndi moyo mwa Mzimu Woyera, tiyeni tiyende pamodzi ndi Mzimu Woyera.
Komabe iwo anawukira ndi kumvetsa chisoni Mzimu Woyera. Motero Yehova anatembenuka nakhala mdani wawo ndipo Iye mwini anamenyana nawo.
Tsono monga Mzimu Woyera akuti, “Lero mukamva mawu ake, musawumitse mitima yanu ngati munachitira pamene munawukira, pa nthawi yoyesedwa mʼchipululu.
Musakhale aulesi mʼmachitidwe anu. Khalani achangu mu mzimu ndipo tumikirani Ambuye.
Musandichotse pamaso panu kapena kuchotsa Mzimu wanu Woyera mwa ine.
Koposa kotani nanga ululu wachilango chimene adzalandire munthu amene amapeputsa Mwana wa Mulungu, amene amayesa magazi a pangano, amene anamuyeretsa, kukhala chinthu chodetsedwa, ndi kunyoza Mzimu wachisomo?
Ndipo potero Ine ndikuwuzani inu, tchimo lililonse ndi cha mwano chilichonse zidzakhululukidwa kwa anthu koma chamwano cha pa Mzimu Woyera, sichidzakhululukidwa.
Koma Petro anamufunsa kuti, “Hananiya, chifukwa chiyani Satana anadzaza chotere mu mtima wako kuti unamize Mzimu Woyera ndipo wapatula ndi kusunga ndalama?