Mavesi a m'Baibulo Onena za Madzi a Moyo

Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Madzi a Moyo oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Yohane 7:38

Malemba kuti ‘Aliyense amene akhulupirira Ine, mitsinje yamadzi amoyo idzatuluka kuchokera mʼkati mwake.’ ”

02 Yohane 4:14

koma aliyense amene adzamwa madzi amene Ine ndidzamupatsa sadzamvanso ludzu. Ndithudi, madzi amene ndidzamupatsa adzakhala kasupe wamadzi wotumphukira ku moyo wosatha.”

03 Yohane 4:10

Yesu anamuyankha kuti, “Koma iwe ukanadziwa mphatso ya Mulungu ndi Iye amene akukupempha madzi akumwa, ukanamupempha ndipo akanakupatsa madzi amoyo.”

04 Yesaya 44:3

Pakuti ndidzathira madzi pa nthaka yowuma, ndi kuyendetsa mitsinje mʼdziko lowuma; ndidzatumiza Mzimu wanga pa ana anu, ndi kutsitsa madalitso anga pa zidzukulu zanu.

Mzimu Woyera ndi mkwatibwi akuti, “Bwerani!” Ndipo amene akumva anena kuti Bwerani! Iye amene ali ndi ludzu abwere, ndipo aliyense amene afuna alandire mphatso yaulere ya madzi amoyo.

06 Yohane 7:37

Pa tsiku lomaliza ndi lalikulu kwambiri laphwando, Yesu anayimirira nafuwula nati, “Ngati munthu ali ndi ludzu, abwere kwa Ine kuti adzamwe.

07 Yeremiya 2:13

“Popeza anthu anga achita machimo awiri: Andisiya Ine kasupe wa madzi a moyo, ndi kukadzikumbira zitsime zawo, zitsime zongʼaluka, zomwe sizingathe kusunga madzi.

08 Masalimo 42:1

Monga mbawala ipuma wefuwefu kufunafuna mitsinje yamadzi, kotero moyo wanga upuma wefuwefu kufunafuna Inu Mulungu.

Mitu yofanana