Mavesi a m'Baibulo Onena za Chizindikiro cha Mzimu

Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Chizindikiro cha Mzimu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Aefeso 1:13

Ndipo inunso pamene munamva mawu a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, munayikidwanso mwa Khristu. Mutakhulupirira, anakusindikizani chizindikiro pokupatsani Mzimu Woyera amene Iye analonjeza.

02 Aefeso 4:30

Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu amene mwasindikizidwa naye chizindikiro cha tsiku la kuwomboledwa.

03 2 Akorinto 1:22

nayikanso Mzimu wake mʼmitima mwathu kutitsimikizira za mʼtsogolo.

04 2 Akorinto 5:5

Tsono ndi Mulungu amene anatikonzeratu ife kuti tilandire zimenezi. Iye anatipatsa Mzimu ngati chikole, kutsimikizira zimene zikubwera.

05 Aroma 8:23

Si zokhazo ayi, ngakhale ife tomwe, amene tili ndi zipatso zoyamba za Mzimu, tikubuwulira mʼkati mwathu pomwe tikudikira mwachidwi kusankhidwa kwathu ngati ana, kuwomboledwa kwa matupi athu.

06 2 Timoteyo 2:19

Komabe maziko olimba, amene Mulungu anawayika ngokhazikika, ndipo mawu olembedwapo ndi awa: “Yehova amadziwa amene ndi ake,” ndiponso, “Aliyense amene amavomereza dzina la Ambuye ayenera kusiya zoyipa.”

07 Yohane 6:27

Gwirani ntchito, osati chifukwa cha chakudya chimene chimawonongeka koma chifukwa cha chakudya chimene sichiwonongeka mpaka ku moyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani. Mulungu Atate anamusindikiza chizindikiro chomuvomereza.”

08 Aroma 8:16

Mzimu mwini amavomerezana ndi mzimu wathu kuti ife ndife ana a Mulungu.

09 1 Yohane 3:24

Iwo amene amamvera malamulo ake amakhala mwa Iye, ndipo Iye amakhala mwa iwo. Ndipo mmenemu ndi momwe timadziwira kuti Iye akukhala mwa ife. Timadziwa mwa Mzimu Woyera amene anatipatsa.

10 Agalatiya 4:6

Ndipo popeza ndinu ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake kuti alowe mʼmitima mwathu, Mzimu amene amafuwula kuti, “Abba, Atate.”

11 Aefeso 4:4

Pali thupi limodzi ndiponso Mzimu mmodzi, monganso pali chiyembekezo chimodzi chimene anakuyitanirani.

12 1 Akorinto 6:11

Ndipo umu ndi mmene ena mwa inu munalili. Koma munatsukidwa, munayeretsedwa, munalungamitsidwa mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu ndi Mzimu wa Mulungu wathu.

Mitu yofanana