Mavesi a m'Baibulo Onena za Pothawira

Mavesi 13 a m'Baibulo onena za Pothawira oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Masalimo 46:1

Mulungu ndiye kothawira kwathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu pa nthawi ya mavuto.

02 Masalimo 62:8

Dalirani Iye nthawi zonse, inu anthu; khuthulani mitima yanu kwa Iye, pakuti Mulungu ndiye pothawirapo pathu. Sela

03 Miyambo 18:10

Dzina la Yehova lili ngati nsanja yolimba; wolungama amathawiramo napulumuka.

04 Masalimo 9:9

Yehova ndiye kothawirako kwa opsinjika mtima, linga pa nthawi ya mavuto.

05 Nahumu 1:7

Yehova ndi wabwino, ndiye kothawirako nthawi ya masautso. Amasamalira amene amamudalira,

06 Masalimo 91:2

Ndidzanena za Yehova, “Iye ndiye pothawira panga ndi linga langa, Mulungu wanga amene ndimadalira.”

07 Masalimo 18:2

Yehova ndiye thanthwe langa, chitetezo changa ndi mpulumutsi wanga; Mulungu wanga ndi thanthwe langa mʼmene ndimathawiramo. Chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa, ndi linga langa.

08 Masalimo 32:7

Inu ndi malo anga obisala; muzinditeteza ku mavuto ndipo muzindizinga ndi nyimbo zachipulumutso. Sela

09 Masalimo 61:3-4

Pakuti Inu mwakhala pothawirapo panga, nsanja yolimba polimbana ndi adani anga. Ine ndikulakalaka kukhala mʼtenti yanu kwamuyaya ndi kupeza chitetezo mu mthunzi wa mapiko anu.

10 Masalimo 142:5

Ndilirira Inu Yehova; ndikuti, “Ndinu pothawirapo panga, gawo langa mʼdziko la anthu amoyo.”

11 Deuteronomo 33:27

Mulungu wamuyaya ndiye pothawirapo pathu, ndipo pa dziko lapansi amakusungani ndi mphamvu zosatha. Adzathamangitsa patsogolo panu mdani wanu, adzanena kuti, ‘Muwonongeni!’

12 Masalimo 31:1-2

Mwa Inu Yehova, ine ndimathawiramo; musalole nʼkomwe kuti ndichititsidwe manyazi; mundipulumutse chifukwa cha chilungamo chanu. Tcherani khutu lanu kwa ine, bwerani msanga kudzandilanditsa; mukhale thanthwe langa lothawirapo, linga lolimba kundipulumutsa ine.

13 2 Samueli 22:3

Mulungu wanga ndiye thanthwe langa, mʼmene ndimathawiramo, chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa. Iye ndi linga langa, pothawirapo panga ndi mpulumutsi wanga. Munandipulumutsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.

Mitu yofanana