Mavesi a m'Baibulo Onena za Lupanga la Mzimu

Mavesi 6 a m'Baibulo onena za Lupanga la Mzimu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Aefeso 6:17

Valani chipewa cha chipulumutso ndi kutenga lupanga la mzimu, limene ndi Mawu a Mulungu.

02 Ahebri 4:12

Paja Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amalowa mpaka molumikizirana moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana fundo ndi mafuta a mʼmafupa. Amaweruza malingaliro ndi zokhumba za mʼmitima.

03 Mateyu 4:4

Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa, ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Mulungu.’ ”

04 Yeremiya 23:29

Kodi suja mawu anga amatentha ngati moto? Suja mawu anga amaphwanya monga ichitira nyundo kuphwanya miyala?” Akutero Yehova.

05 Masalimo 119:11

Ndasunga mawu anu mu mtima mwanga kuti ndisakuchimwireni.

06 Chivumbulutso 1:16

Mʼdzanja lake lamanja ananyamula nyenyezi zisanu ndi ziwiri, ndipo mʼkamwa mwake munali lupanga lakuthwa konsekonse. Nkhope yake imawala ngati dzuwa lowala kwambiri.

Mitu yofanana