Mavesi a m'Baibulo Onena za Zida za Mulungu
Mavesi 9 a m'Baibulo onena za Zida za Mulungu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Valani zida zonse za Mulungu kuti muthe kuyima ndi kukana machenjerero a Satana.
Choncho valani zida zonse za Mulungu, kuti pamene tsiku loyipa kwambiri lifika, mudzathe kuyima chilili, ndipo mutatha kuchita zonse, mudzayimabe mwamphamvu.
Tsono imani mwamphamvu, mutamangira choonadi ngati lamba mʼchiwuno mwanu, mutavala chilungamo ngati chitsulo chotchinjiriza pa chifuwa. Valani Uthenga Wabwino wamtendere ku mapazi anu ngati nsapato.
Kuwonjezera pa zonsezi, nyamulani chishango cha chikhulupiriro, ndipo ndi chimenechi mudzatha kuzimitsa mivi yonse yoyaka moto ya oyipayo.
Pakuti zida zathu zankhondo si zida za dziko lapansi. Koma ndi mphamvu zochokera kwa Mulungu zotha kugwetsa malinga.
Pakuti sitikulimbana ndi thupi ndi magazi, koma tikulimbana ndi maufumu, maulamuliro, mphamvu za dziko la mdima, ndi mphamvu zoyipa kwambiri zauzimu zamlengalenga.
Ndipo mupemphere mwa Mzimu nthawi zonse, mʼmitundu yonse ya mapemphero ndi zopempha. Ndipo pozindikira izi, khalani achangu kupempherera oyera mtima nthawi zonse.
Usiku watsala pafupifupi kutha. Kwatsala pangʼono kucha. Tiyeni tsono tichotse ntchito zamdima ndipo tivale chovala chakuwunika.
Koma popeza ndife a usana, tikhale odzisunga, titavala chikhulupiriro ndi chikondi ngati chovala pachifuwa, ndi chiyembekezo cha chipulumutso ngati chipewa.